SPEECH BY HIS EXCELLENCY DR. LAZARUS McCARTHY CHAKWERA DURING THE NATIONAL MEMORIAL SERVICE IN HONOUR OF THE 9 VICTIMS OF THE 10 JUNE 2024 MDF PLANE CRASH
10 June 2025

SPEECH BY HIS EXCELLENCY DR. LAZARUS McCARTHY CHAKWERA, PRESIDENT OF THE REPUBLIC OF MALAWI DURING THE NATIONAL MEMORIAL SERVICE IN HONOUR OF THE 9 VICTIMS OF THE 10 JUNE 2024 MDF PLANE CRASH
NTHUNGWA, MALAWI
TUESDAY, 10TH JUNE 2025
Amayi ndi Abambo,
Tasonkhana malo ano lero ngati aMalawi ndi cholinga choti tikumbukire abale athu asanu ndi anayi omwe anataya myoyo yawo pangozi yandege ya ku Malawi Defense Force yomwe inagwera kuno pa 10 June chaka chatha. Ndinakakonda kuti tinakakhala ndi kuthekera kopanga mwambo oterewu ku malo onse 9 komwe tinaika maliro a anthu onse omwe anatisiya pa ngozi imeneyi, ndiye ndithokoze onse amene apanga zotheka kuti ku malo ena komwe kunagonera abale athuwa kukhalenso miyambo yapadela kuyambira lero mpaka masiku amene akubwera kutsogoloku.
Ndiye kaya tasonkhana kuno komwe kunachitikira ngoziyo kaya kaya tasonkhana komwe anthuwa anaikidwa, chachikulu ndi chokuti tonse ngati aMalawi tiri limodzi pokumbukira malemu Vice President Dr. Saulos Klaus Chilima ndi anthu ena 8 omwe anatisiya mwadzidzi pa 10 June chaka chatha.
Kukumbukira kwathu kwa lero tonse ndikofunikira kwambiri muulendo wathu ofuna kupeza chitonthozo kuululu omwe timaumvabe mmitima mpaka lero. Choyambilira chofunika pa ulendo umeneu ofunafuna chitonthozo ndi kupatsana mpata olira mwa chisoni pangozi yomwe inachitikai. Iyiyi inali ngozi yoopsya, yopangitsa mantha, yosowetsa mtendere, yoswetsa mitima, komanso yothetsa nzeru zathu zaumunthu. Iyiyi inali ngozi yopweteka kwambiri, ndipo ndikoyenera kulolerana kulira chifukwa mu misozi yathu ndi mankhwala paokha achitonthozo.
Chachiwiri chofunika pa ulendo umeneu ofunafuna chitonthozo ndi kupuputana misoziyo popepesana ndi kutonthozana. Malemu Dr. Saulos Klaus Chilima ndi anthu ena 8 omwe anafa pangozi imeneyi anali aMalawi okondeka komanso ofunikira ku mabanja awo, azibale awo, ogwira ntchito nawo, opemphela nawo, azinzawo ocheza nawo, othandizidwa nawo, komanso aMalawi onse owadziwa ndi owafunira zabwino.
Onsewa ndi anthu oti imfayi imawawawa tsiku ndi tsiku, ndipo tonse tiyenera kuchita mbali yathu kuti titonthozane munjira zosiyanasiyana, chifukwa patsiku lomwe ngoziyi inachitika, tinathyoka ngati dziko, ndipo tonse tikuyenera kutonthozana chifukwa Mulungu amatiphunzitsa kuti Odala ali iwo achifundo chifukwa ndaonso azachitilidwa chifundo.
Ndiye ndikuthokozeni aMalawi nonse amene mwakhala mukugwira ntchito imeneyi yotonthozana, komanso ndikuthokozeni nonse amene mwakhala mukuyesetsa kupewa kugwa mmayesero ofuna kusupula mabala a aMalawi anzanu omwe naonso anasweka mitima ndi ngozi imeneyi, makamaka mayesero ofuna kusupula mabala amabanja oferedwa polowetsa ndale pa imfa ya azibale awo. Ife mbali yathu ndikutonthozana kuti tipuputane misozi ndikuuzilirana mabala omwe tili nawo.
Chachitatu chofunika pa ulendo umeneu ofunafuna chitonthozo ndi kupemphelerana. Moyo wathu anatipatsa ndi Mulungu, ndipo palibe mmodzi waife amene saadzatsikira kwa chete. Imfa iliyonse ingatigwere ndichikumbutso cha umunthu wathu, chifukwa anthufe timayenda ndi moyo obwereka, moyo omwe mwini wake namalenga anaulembela malire oti sitimawadziwa ndi komwe. Tsiko lomwe tidzafele sitimalidziwa. Malo omwe tidzafele sitimawadziwa. Njira yomwe tidzafele sitimaidziwa. Msinkhu omwe tidzafele sitimaudziwa.
Ndiye imfa ikatigwera ndi chanzeru kukhala pansi modzichepetsa pa maso a Yehova nkupemphelerana kuti tikhale anthu odziwa kuwerenga masiku athu, anthu ogwiritsa ntchito bwino masiku omwe tili nawo mdziko muno, komanso anthu okhazikika mwa Yesu chifukwa sikale lomwe tonse nthawi idzatikwanile yopuma mpweya wathu otsiriza nkusiya zonse zadziko lapansi kuti time pamaso aMulungu kukapereka ripoti ya moyo wathu.
Ndiye ndikuthokozeni inu amipingo potilalikira ndi kutipemphelera lero kuti tikhale anthu ogwiritsitsa cha muyaya osati kumangoyenda ngati kuti pa dziko pano pali chathu cheni cheni, chifukwa zo ona zake nzakuti onse omwe timawakonda mdziko muno ndi zonse zomwe tili nazo mdziko muno sitizatenga pa tsiko la imfa yathu. Chuma chomwe tingatenge ndi ubale wathu ndi Mulungu basi, ndiye mapemphero ngati awa ndi ofunika kwambiri.
Chachinayi chofunika pa ulendo umeneu ofunafuna chitonthozo ndi kulemekeza abale amene anatisiyawa. Palibepo olo mmodzi pa anthu amenewa amene anali osafunika. N’chifukwa chake Abusa a Nyirenda atifotokozela mbiri ya wina aliyense amene anatisiya pangozi imenei. Palibepo olo mmodzi yemwe saakuyenera kupatsidwa ulemu oyenelera.
Palibepo olo mmodzi yemwe akuyenera kunyozedwa kapena kupeputsidwa. Moyo wa munthu aliyense ndi mphatso ya mtengo wapatali. Malemu Dr. Saulos Klaus Chilima anali munthu wanzeru, olimbikira ntchito, okonda dziko lake, odzipereka kubanja lake, olemekeza aliyense paudindo pake, komanso anali Vice President wa aMalawi tonse, ndiye sikulakwa kumulemekeza.
Komanso anthu 8 omwe anafela nawo limodzi saakanapezeka mu ndege imeneyi akanakhala kuti anali anthu osafunika kapena opanda phindu, ndiye sikulakwa naonso kuwalemekeza limodzi malo omwe anatayila miyoyo yawo pamodzi ndi a Vice President athu. Kulemekeza anthu omwe anatisiya kumabweretsa chitonthozo chapadela. Ndipo mbali imodzi yowalemekeza anthu amenewa ndi kuonetsetsa kuti mabanja awo omwe anawasiya tiwasamalire.
Ndi chifukwa chake mabanja onsewo ine ndinawaitana paokhapaokha kuti ndimve kuti miyoyo yao iri bwanji, ndipo madando awo onsewo ndinawamva, komanso a SPC ndinawapatsa mpaka kumapeto kwa mwezi uno kuti madando amenewo awalongosole chifukwa sindikufuna kuti mabanja oferedwa azikhala okhumudwa ndi zinthu zoti tikuyenera kuchita kuti tiwasamale, chifukwa kusamalira mabanja amenewa ndi njira imodzi yolemekeza anthu amene anatisiyawa.
Komanso, malemu a Vice President Chilima ndi munthu yemwe anali wamkulu mdziko muno, ndiye ndikoyenela kuwalemekeza mwapadela. Pachifukwa ichi ndasankha kuti nseu wapamwamba wa 6 lane omwe boma lathu lamanga ku Lilongwe upatsidwe dzina la Chilima polemekeza gawo lomwe anatenga polimbikitsa umodzi wathu pachitukuko cha dziko kusiyana ndi ndale zogawa dziko.
Chotsiriza chofunika paulendo wathu ofunafuna chitonthozo ngati dziko ndikutengerapo maphunziro pazonse zomwe zaonekela poyera kudzera mma ripoti ufufuza zomwe zanapangitsa ngozi imeneyi. Chichitikire ngozi imeneyi chaka chatha patuluka ma ripoti atatu. Ripoti yoyamba anatulutsa ndi madokotala omwe anapima matupi a anthu omwe anamwalirawa mu June chaka chatha, omwe anatitsimikizira kuti ngozi imeneyi palibe anapanga survive.
Ripoti yachiwiri anatulutsa ndi a Commission of Inquiry mu December chaka chathachi, omwe anafufuza kagwiridwe kantchito a ma agency osiyanasiyana patsiku lomwe ndege inagwa komanso tsiku lomwe inapezeka. Ripoti yachitatu ndi yomwe atulutsa loweruka lapitali ma Investigator a ku Germany, kufotokoza zomwe zinalakwika mu kasamaliridwe ndi kayendetsedwe ka denge imeneyi pa tsiku loti nyengo siinali bwino komanso loti ulendowo suunakonzekeredwe mokwanila.
Ndiye poti ma ripoti onsewa atulukano, zonsezi ndi zinthu zoti ndikuzilingalira tsopano kuti monse momwe munalakwika tikonzemo, chifukwa kupanda kutengerapo phunziro lokonza zinthu pangozi imeneyi ndiye kuti sitichita bwino ngati dziko. Ndiye masiku akubwerawa ndifotokoza zonse zomwe nditasinthe pogwiritsa ntchito mauphungu onse omwe abwera kudzera mma ripoti atatu amenewa.
Komano ndikuthokozeni nonse amene mwatengapo gawo kuti ma ripoti amenewa amalizike mu nthawi yake, kuphatikizapo inu a boma la ku Germany omwe mwationetsa chikondi pofufuza kuti chinachitika ndi chani kuti ndege imenei igwe nkutitengela miyoyo yofunika ngati imenei.
Ndikudziwa kuti chichitikire ngozi imenei panenedwa zambiri zosakhala bwino komanso zabodza, koma ndikufuna ndikupempheni nonse aMalawi kuti mukhululukirane chifukwa nkhondo siimanga mudzi. Komanso ndikufuna ndikuthokozeni aMalawi nonse posankha kuima limodzi tsiku la lero kuti tonse tilire limodzi. Zikomo akumabanja oferedwa omwe muli pano.
Zikomo ansembe ampingo wa chikatolika ndi amipingo ina ndi zipembedzo zina omwe muli pano. Zikomo inu a Ngwenyama Paramount Chief Gomani V omwe mwachokera ku Ntcheu, kwawo kwamalemu Vice President Chilima, komanso inu a Ngwenyama Paramount Chief M’mbelwa V omwe mwatilandira kuno ku Mzimba, ndi mafumu athu onse akuluakulu omwe muli pano.
Zikomo inu ogwira ntchito zaboma omwe muli pano. Zikomo inu Olemekezeka a Atupele Muluzi, omwe muli mtsogoleri wa chipani cha United Democratic Front, komanso zikomo atsogoleri azipani zosiyasiyana omwe muli pano. Zikomo inu akazembe onse a maiko ena omwe muli pano.
Zikomo inu aMalawi nonse komwe muli omwe mukulondola mwambo omwe uli pano. Monga mtsogoleri yemwe manamusankha kuti akutumikireni mu nyengo zonse, ndikuti pepani, pepani, pepani nonse.
Ambuye akudalitseni, komanso adalitse dziko lathu la Malawi, ndipo apitilize kutisunga mu mtendere. Zikomo.